-
Ekisodo 10:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Atatero Yehova anasintha mphepo yamphamvuyo kuti iziwomba kuchokera kumadzulo ndipo inatenga dzombelo ndi kulithira m’Nyanja Yofiira. Motero m’dera lonse la Iguputo simunatsale dzombe ngakhale limodzi.
-
-
Yesaya 50:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 N’chifukwa chiyani nditabwera sindinapeze aliyense?+ N’chifukwa chiyani nditaitana palibe amene anayankha?+ Kodi dzanja langa lafupika kwambiri moti silingathe kuwombola,+ kapena kodi mwa ine mulibe mphamvu zopulumutsira? Inetu ndimaumitsa nyanja+ pongoidzudzula chabe.+ Mitsinje ndimaisandutsa chipululu.+ Nsomba zake zimanunkha chifukwa chakuti mulibe madzi ndipo zimafa ndi ludzu.+
-