9 Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+
28 Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo, mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake, atsogoleri ake onse ndi madera onse olamulidwa ndi aliyense wa amenewa.