15 Yehova adzaphwetsa chigawo cha nyanja ya Iguputo,+ ndipo adzayendetsa dzanja lake moopseza Mtsinje+ pogwiritsa ntchito mpweya wake wotentha. Adzamenya mtsinjewo pokwapula timitsinje take 7, ndipo adzachititsa anthu kuwolokapo nsapato zili kuphazi.+