10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+
11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+