17 Pamenepo Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova Mulungu wa makamu,+ Mulungu wa Isiraeli,+ wanena kuti, ‘Mukadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzinda uwu sadzautentha, komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+