2 Deralo lidzachitadi maluwa.+ Lidzasangalala ndipo lidzakondwera n’kufuula ndi chisangalalo.+ Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni+ ndi kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+ Padzakhala anthu amene adzaone ulemerero wa Yehova+ ndi kukongola kwa Mulungu wathu.+