6 pamenepo ine ndidzachititsa nyumba iyi kukhala ngati nyumba ya ku Silo.+ Ndipo mzinda uwu ndidzausandutsa chinthu chotembereredwa pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.’”’”+
22 Anthu onse a ku Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, potemberera ena azidzatchula za Zedekiya ndi Ahabu kuti: “Yehova akuchititse kukhala ngati Zedekiya ndi Ahabu+ amene mfumu ya Babulo inawawotcha pamoto!”+