19 chifukwa chakuti mtima wako+ unali wofewa ndipo unadzichepetsa+ chifukwa cha Yehova utamva zimene ndanena zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti malowa adzakhala chodabwitsa ndi temberero,+ unang’amba+ zovala zako n’kuyamba kulira pamaso panga, ineyo ndamva,” ndiwo mawu a Yehova.+