Levitiko 26:40 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 40 Chotero adzavomereza kuti iwo komanso makolo awo anayenda motsutsana nane,+ anandichimwira+ ndi kundichitira mosakhulupirika. 1 Mafumu 21:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Popeza wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake.+ M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.”+ Mika 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+ Yakobo 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+
40 Chotero adzavomereza kuti iwo komanso makolo awo anayenda motsutsana nane,+ anandichimwira+ ndi kundichitira mosakhulupirika.
29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga?+ Popeza wadzichepetsa chifukwa cha ine, sindidzabweretsa tsokali m’masiku ake.+ M’malomwake, ndidzalibweretsa panyumba yake m’masiku a mwana wake.”+
8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+
6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+