17 “Ine ndinakwiya chifukwa cha phindu lachinyengo limene analipeza mosayenera.+ Ndinakwiya ndipo ndinamulanga. Ndinabisa nkhope yanga chifukwa cha mkwiyo.+ Koma iye ankangoyendabe ngati wopanduka+ m’njira ya mtima wake.
22 Anthu anga ndi opusa.+ Iwo sanaganizire za ine.+ Iwo ndi ana opanda nzeru ndipo sazindikira kalikonse.+ Iwo ndi anzeru pa kuchita zoipa koma sadziwa kuchita zabwino.+