4 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo+ ana a Isiraeli pamodzi ndi ana a Yuda adzabwera,”+ watero Yehova. “Iwo adzayenda akulira+ ndipo adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+
11 Pamenepo ana a Yuda ndi ana a Isiraeli adzasonkhanitsidwa pamodzi ndipo adzakhala ogwirizana.+ Iwo adzadziikira mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka m’dzikolo,+ chifukwa tsikuli lidzakhala lofunika kwambiri kwa Yezereeli.*+