Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pofika mwezi wa 7,+ ana a Isiraeli anali akukhala m’mizinda yawo. Ndiyeno anthuwo anayamba kusonkhana ku Yerusalemu+ monga munthu mmodzi.+

  • Yesaya 11:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu n’kusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumalekezero anayi a dziko lapansi.+

  • Yeremiya 3:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “M’masiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli,+ ndipo onse+ adzatuluka m’dziko la kumpoto ndi kulowa m’dziko limene ndinapereka kwa makolo anu monga cholowa chawo.+

  • Yeremiya 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+

  • Ezekieli 37:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndiyeno uziike pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi. Chotero ndodozo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja lako.+

  • Mika 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.+ Ndidzasonkhanitsa otsala a Isiraeli.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa m’khola, komanso ngati gulu la ziweto limene lili pamalo amsipu.+ Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+

  • Aroma 11:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena