-
Yesaya 66:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ monga mphatso kwa Yehova.+ Adzayenda pamahatchi, pangolo, pangolo zotseka pamwamba, panyulu,* ndi pangamila zazikazi zothamanga,+ popita kuphiri langa loyera,+ ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene ana a Isiraeli amabweretsera mphatso m’nyumba ya Yehova, ataiika m’chiwiya choyera,”+ watero Yehova.
-
-
Obadiya 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Anthu amene anatengedwa kupita kudziko lina kuchokera pachiunda ichi chomenyerapo nkhondo,+ amene ndi ana a Isiraeli, adzatenga zinthu zimene zinali za Akanani+ mpaka kukafika ku Zarefati.+ Anthu amene anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu kupita kudziko lina, amene anali ku Sefaradi, adzatenga mizinda ya Negebu kukhala yawo.+
-