3 Pakuti iwe udzafutukukira mbali ya kudzanja lamanja ndi kumanzere, ndipo ana ako+ adzalanda ngakhale mitundu ya anthu.+ Iwo adzakhala m’mizinda imene inasiyidwa yabwinja.+
4 “Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe.+ Kuchokera kutali, ana ako aamuna akubwera limodzi ndi ana ako aakazi, amene adzasamalidwe atanyamulidwa m’manja.+
31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga,+ ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake+ kuchokera kumphepo zinayi,+ kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.