Ezara 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+ Yesaya 27:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 M’tsiku limenelo kudzalira lipenga lomveka kutali.+ Ndiyeno anthu amene akuwonongeka m’dziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana m’dziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira+ Yehova m’phiri loyera ku Yerusalemu.+ Yesaya 35:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo. Yesaya 48:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+ Yesaya 49:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.” Yeremiya 31:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Udziikire zizindikiro za mumsewu. Udziikire zikwangwani.+ Ika mtima wako panjirayo, njira imene uyenera kuyendamo.+ Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.+
3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+
13 M’tsiku limenelo kudzalira lipenga lomveka kutali.+ Ndiyeno anthu amene akuwonongeka m’dziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana m’dziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira+ Yehova m’phiri loyera ku Yerusalemu.+
8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo.
20 Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+
12 Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.”
21 “Udziikire zizindikiro za mumsewu. Udziikire zikwangwani.+ Ika mtima wako panjirayo, njira imene uyenera kuyendamo.+ Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.+