6 Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+ Ndidzawachitira chifundo ndipo ndidzawapatsa malo okhala.+ Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+ Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.+