14 Chotero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani, ndi Asaya anapita kukalankhula ndi Hulida mneneri wamkazi.+ Hulida anali mkazi wa Salumu yemwe anali wosamalira zovala, mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi,+ ndipo Hulidayo anali kukhala kumbali yatsopano ya mzinda wa Yerusalemu.+