12 Pamenepo anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda chodyera cha mlembi, kumene akalonga onse anali atakhala pansi. Kumeneko kunali Elisama+ mlembi, Delaya+ mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya+ mwana wa Safani,+ Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse.