7 Ndiyeno khoma la mzindawo linabooledwa,+ ndipo amuna onse ankhondo anayamba kuthawa.+ Iwo anatuluka mumzindawo usiku kudzera pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu,+ ndipo analowera njira yopita ku Araba. Apa n’kuti Akasidi atazungulira mzinda wonsewo.+