14 “Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri+ ndi a Amaakati,+ ndipo midzi ya ku Basana imeneyo anaitcha dzina la iye mwini lakuti, Havoti-yairi*+ kufikira lero.
5 Anali kulamulira kuphiri la Herimoni,+ ku Saleka, ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri+ ndi Amaakati.+ Anali kulamuliranso hafu ya Giliyadi, mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni,+ mfumu ya Hesiboni,+ anali kulamulira.