Yeremiya 21:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Anthu amene adzakhalabe mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.+ Koma amene adzatuluka ndi kugwidwa ndi Akasidi amene akuzungulirani adzakhala ndi moyo. Iwo adzapulumutsa moyo wawo.”’+ Yeremiya 24:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+ Yeremiya 43:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+
9 Anthu amene adzakhalabe mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.+ Koma amene adzatuluka ndi kugwidwa ndi Akasidi amene akuzungulirani adzakhala ndi moyo. Iwo adzapulumutsa moyo wawo.”’+
10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+
11 Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+