59 Yehova adzakulitsa kwambiri miliri yako ndi miliri ya ana ako. Miliri imeneyo idzakhala yaikulu kwambiri ndi yokhalitsa,+ ndipo udzagwidwa ndi matenda onyansa ndi okhalitsa.+
15 Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+