Oweruza 6:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+ Oweruza 7:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Tsopano Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa,+ anaphimba chigwa chonse chifukwa cha kuchuluka kwawo ngati dzombe.+ Ngamila zawo+ zinali zosawerengeka, zochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. Nahumu 3:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Alonda ako ali ngati dzombe ndipo akapitawo ako olemba anthu usilikali ali ngati gulu la dzombe. Pa tsiku lozizira limabisala m’makoma. Dzuwa likawala, dzombelo limauluka ndi kuthawira kutali ndipo silidziwika kuti lili kuti.+
5 Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+
12 Tsopano Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa,+ anaphimba chigwa chonse chifukwa cha kuchuluka kwawo ngati dzombe.+ Ngamila zawo+ zinali zosawerengeka, zochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.
17 Alonda ako ali ngati dzombe ndipo akapitawo ako olemba anthu usilikali ali ngati gulu la dzombe. Pa tsiku lozizira limabisala m’makoma. Dzuwa likawala, dzombelo limauluka ndi kuthawira kutali ndipo silidziwika kuti lili kuti.+