4 Chita manyazi iwe Sidoni,+ ndiponso iwe malo achitetezo a m’mbali mwa nyanja, chifukwa nyanja yanena kuti: “Sindinamvepo zowawa za pobereka, ndipo sindinaberekepo. Sindinalerepo anyamata kapena anamwali.”+
3 Kenako, uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya ana a Amoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene akubwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda.