13 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti ana a Amoni+ andipandukira mobwerezabwereza, sindidzawasinthira chigamulo changa.+ Sindidzawasinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi ndi cholinga chakuti afutukule malo awo okhala.+