15 Pakuti unali kusangalala chifukwa chakuti cholowa cha nyumba ya Isiraeli chinawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri ndiponso Edomu yense, mudzasanduka bwinja,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+