Miyambo 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+ Maliro 4:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+ Obadiya 12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka.+ Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.+ Sunayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene iwo anamva zowawa. Obadiya 15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Tsiku la Yehova limene adzawononge mitundu yonse ya anthu lili pafupi.+ Iwe adzakuchitira zofanana ndi zimene wachitira m’bale wako.+ Zimene unachita zidzabwerera pamutu pako.+
5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anam’panga.+ Amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+
21 Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+
12 “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka.+ Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.+ Sunayeneranso kulankhula modzitama pa tsiku limene iwo anamva zowawa.
15 Tsiku la Yehova limene adzawononge mitundu yonse ya anthu lili pafupi.+ Iwe adzakuchitira zofanana ndi zimene wachitira m’bale wako.+ Zimene unachita zidzabwerera pamutu pako.+