6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
7 Yehova akuwabweretsera+ Mtsinje*+ wa madzi ambiri ndi amphamvu, womwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse.+ Iyo idzadzaza timitsinje take tonse n’kusefukira mpaka m’mphepete mwa mitsinje yake yonse,