12 Kenako ndinapereka chikalata cha pangano chogulira mundawo kwa Baruki+ mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya. Ndinamupatsa chikalata chimenechi pamaso pa Hanameli mwana wa m’bale wa bambo anga, pamaso pa mboni zimene zinasaina chikalatacho+ ndi pamaso pa Ayuda onse amene anali m’Bwalo la Alonda.+