Yesaya 22:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 N’chifukwa chake ndanena kuti: “Musandiyang’anitsitse. Ine ndikulira mopwetekedwa mtima+ ndipo anthu inu musaumirire kunditonthoza pamene ndikulirira mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe walandidwa katundu.+ Yeremiya 13:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina. Maliro 2:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda.
4 N’chifukwa chake ndanena kuti: “Musandiyang’anitsitse. Ine ndikulira mopwetekedwa mtima+ ndipo anthu inu musaumirire kunditonthoza pamene ndikulirira mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe walandidwa katundu.+
17 Ndipo ngati simudzamvera mawu ake+ ndidzalira ndi kugwetsa misozi m’malo obisika chifukwa cha kunyada kwanu. Maso anga adzatulutsa misozi+ chifukwa chakuti nkhosa+ za Yehova zidzakhala zitagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.
11 Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda.