19 M’mimba mwanga ine, m’mimba mwanga! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.+ Mtima wanga ukuvutika.+ Sindingathe kukhala chete pakuti ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.+
9Ndikanakonda kuti m’mutu mwanga mukhale madzi ambiri ndiponso kuti maso anga akhale magwero a misozi.+ Pamenepo ndikanalira usana ndi usiku chifukwa cha anthu ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga.+