36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano n’kachiwiri akundichenjerera amene uja!+ Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo? Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye anapitiriza kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?”