Yeremiya 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+ Yeremiya 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu. Yeremiya 6:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. Pali mtundu wamphamvu umene udzadzutsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Habakuku 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ine ndikuutsa Akasidi,+ mtundu waukali ndi waphuma umene ukupita kumalo otakasuka a padziko lapansi kukatenga malo amene si awo.+
15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+
6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu.
22 Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. Pali mtundu wamphamvu umene udzadzutsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
6 Ine ndikuutsa Akasidi,+ mtundu waukali ndi waphuma umene ukupita kumalo otakasuka a padziko lapansi kukatenga malo amene si awo.+