-
Yeremiya 21:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu onse, onse opulumuka ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu mumzinda uwu, ndidzawapereka m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo. Ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa amene akufuna moyo wawo. Nebukadirezara adzawapha ndi lupanga+ ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+
-
-
Yeremiya 25:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ watero Yehova, “ndipo ndikuitananso Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mtumiki wanga.+ Ndikuitana anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu okhala mmenemo, komanso kuti aukire mitundu yonse yokuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani, ndi kukusandutsani chinthu chodabwitsa chimene azidzachiimbira mluzu+ ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.+
-