6Bisalani, inu ana a Benjamini, thawani pakati pa Yerusalemu. Ku Tekowa+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Ku Beti-hakeremu+ kwezani moto wa chizindikiro, chifukwa chiwonongeko chachikulu, tsoka, lasuzumira kuchokera kumpoto.+
9 Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+