7 Mfumu ya Iguputo sinatulukenso+ m’dziko lake,+ chifukwa mfumu ya Babulo inali itatenga zinthu zonse zomwe zinali za mfumu ya Iguputo,+ kuyambira kuchigwa*+ cha Iguputo kukafika kumtsinje wa Firate.+
16 Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani.+ Dziko lonse layamba kugwedezeka chifukwa cha phokoso la kulira kwa mahatchi ake amphongo.+ Adani akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zokhala mmenemo, mzinda ndi onse okhala mmenemo.”