21 Solomo anakhala wolamulira wa maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumu amenewa anali kubweretsa mphatso kwa Solomo ndi kum’tumikira masiku onse a moyo wake.+
12 Inu ana a Isiraeli, monga momwe munthu amathyolera zipatso mumtengo n’kuzisonkhanitsa+ pamodzi chimodzi ndi chimodzi, Yehova adzakusonkhanitsani inu+ amene mwamwazikana m’dera loyambira ku Mtsinje*+ mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+