Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 15:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+

  • Ekisodo 23:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+

  • Deuteronomo 11:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Malo alionse amene mapazi anu adzapondapo adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja ya kumadzulo.+

  • 2 Samueli 8:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Davide anapha Hadadezeri,+ mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukabwezeretsa ulamuliro wake kumeneko.

  • 1 Mbiri 19:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Asiriya ataona kuti agonjetsedwa+ ndi Aisiraeli, anatumiza amithenga kukaitana Asiriya amene anali m’dera la ku Mtsinje,*+ pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa gulu lankhondo la Hadadezeri.

  • Salimo 72:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+

      Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena