Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “Dziko limene ndidzakupatsa lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita izi, chifukwa anthu okhala m’dzikomo ndidzawapereka m’manja mwako, ndipo iwe udzawathamangitsa pamaso pako.+

  • 1 Mafumu 4:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Solomo anakhala wolamulira wa maufumu onse kuyambira ku Mtsinje*+ mpaka kudziko la Afilisiti, n’kukafika kumalire ndi Iguputo. Maufumu amenewa anali kubweretsa mphatso kwa Solomo ndi kum’tumikira masiku onse a moyo wake.+

  • Salimo 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Tandipempha,+ ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako,+

      Ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.+

  • Salimo 89:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ndinaika ulamuliro wake panyanja,+

      Ndipo ndinam’patsa ulamuliro pamitsinje.+

  • Zekariya 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndidzawononga magaleta ankhondo mu Efuraimu ndiponso mahatchi mu Yerusalemu.+ Mauta omenyera nkhondo+ adzathyoledwa. Mfumuyo idzalankhula mawu amtendere kwa anthu a mitundu ina.+ Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja. Ndiponso udzachokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena