-
Yeremiya 37:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya. Atabwera naye, mfumuyo inayamba kumufunsa mafunso m’nyumba mwake pamalo obisika.+ Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Pamenepo Yeremiya anayankha kuti: “Inde alipo!” Ndiyeno Yeremiya ananenanso kuti: “Inuyo mudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Babulo!”+
-