19 Kodi Yuda mwamukaniratu,+ kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+ N’chifukwa chiyani mwatikantha popanda wotichiritsa?+ Anthu anali kuyembekezera mtendere, koma palibe chabwino chimene chachitika. Anali kuyembekezera nthawi yochiritsidwa, koma taonani, kukuchitika zoopsa zokhazokha.+