2 Koma msilikali wothandiza mfumu amene anaigwira ndi dzanja lake,+ anayankha munthu wa Mulungu woonayo, kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba,+ kodi zimenezo zingachitike?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako,+ koma sudya nawo.”+