10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu waukulu ngati mkazi amene akumva kupweteka kwambiri pobereka.+ Tsopano uchoka m’tauni ndipo ukakhala kumudzi.+ Ukafika mpaka ku Babulo+ koma kumeneko udzapulumutsidwa.+ Kumeneko Yehova adzakuwombola m’manja mwa adani ako.+