14 Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, tilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+
5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+