-
Ezekieli 23:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Onsewa adzabwera kudzakuukira. Anthuwo pofika, padzamveka phokoso la magaleta* ankhondo ndi la mawilo.+ Iwo adzabwera ndi khamu la anthu, atatenga zishango zazikulu, zishango zazing’ono ndi zisoti. Iwo adzakuzungulira kuti akuukire. Ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, ndipo adzakuweruza motsatira malamulo awo.+
-