7 Madambo a m’mphepete mwa mtsinje wa Nailo, malo othera mtsinje wa Nailo, ndi malo onse obzala mbewu m’mphepete mwa mtsinjewo, adzauma.+ Zomera za m’mphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo.
12 Ndidzaumitsa ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo+ ndi kugulitsa dzikolo kwa anthu oipa.+ Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu achilendo.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’+