Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 30:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+

  • Yeremiya 46:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope ndipo usagwidwe ndi mantha, iwe Isiraeli.+ Pakuti ine tsopano ndikukupulumutsa kuchokera kutali. Mbewu yako ndikuipulumutsa kuchokera m’dziko limene iwo anali akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndi kukhala mwabata ndiponso mosatekeseka, popanda womuopsa.+

  • Ezekieli 28:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

  • Zefaniya 3:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Pa nthawi imeneyo ndidzakubwezaninso kunyumba anthu inu. Ndithu, pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani pamodzi. Ndidzakuchititsani kukhala otchuka komanso otamandidwa pakati pa mitundu yosiyanasiyana padziko lapansi. Zimenezi zidzachitika ndikadzabwezeretsa pamaso pako anthu ako amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo,” watero Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena