6 Chipinda cham’mbali chapansi chinali mikono isanu m’lifupi mwake. Chipinda cham’mbali chapakati chinali mikono 6 m’lifupi mwake, ndipo chipinda cham’mbali chachitatu chinali mikono 7 m’lifupi mwake. Makoma onse akunja a nyumbayo anangowagoba+ n’cholinga choti asawaboole.+