15 Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga* anakutamo ndi matabwa. Kenako anakuta pansi pa nyumbayo ndi matabwa akuluakulu a mitengo yofanana ndi mkungudza.+
5 Nyumba yaikuluyo anaikuta+ ndi matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi zithunzi za mitengo yakanjedza+ zojambula mochita kugoba ndiponso matcheni.+