9 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!’+
“‘Siyani ziwawa ndi kulanda zinthu za anthu anga.+ Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.